-
Yeremiya 26:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 “Mika+ wa ku Moreseti+ nayenso anali kunenera m’masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda.+ Iye anauza anthu onse a mu Yuda kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ziyoni adzagawulidwa ngati munda,+ ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.”’+
-
-
Ezekieli 24:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 ‘Uza nyumba ya Isiraeli kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidetsa malo anga opatulika,+ chinthu chimene mumachinyadira kwambiri,+ chinthu chosiririka kwa inu,+ ndiponso chinthu chimene mumachichitira chifundo. Ana anu aamuna ndi aakazi amene munawasiya m’mbuyo adzaphedwa ndi lupanga.+
-