4 Iwe udzafera m’mapiri a ku Isiraeli+ limodzi ndi magulu ako onse a asilikali ndi anthu a mitundu ina amene adzakhale nawe. Ndidzakuperekani kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire kuti mukhale chakudya chawo.”’+
18 kuti mudzadye minofu+ ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi+ ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”