Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 29:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Yehova wanena kuti: “Popeza anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha+ koma mtima wawo auika kutali ndi ine,+ ndiponso amangophunzira malamulo a anthu n’kumaganiza kuti kuchita zimenezo ndiye kundiopa,+

  • Yeremiya 6:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yehova wauza anthuwo kuti: “Imani chilili panjira anthu inu, kuti muone ndi kufunsa za njira zakale, kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino.+ Mukaipeza muyende mmenemo+ kuti mupeze mpumulo wa miyoyo yanu.”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitiyendamo.”+

  • Yeremiya 44:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ife tichita zonse zimene tanena.+ Tipereka nsembe zautsi ndi kuthira nsembe zachakumwa+ kwa ‘mfumukazi yakumwamba.’+ Tichita zimenezi monga mmene ife,+ makolo athu,+ mafumu athu+ ndi akalonga athu anachitira m’mizinda ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu pamene tinali kudya mkate ndi kukhuta ndipo zinthu zinali kutiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse.+

  • Mateyu 7:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita+ chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.+

  • Luka 6:49
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 49 Koma amene akumva ndi kusachita,+ ali ngati munthu womanga nyumba yopanda maziko padothi. Apanso mtsinje unasefukira n’kuwomba nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo inagwa, mwakuti kugwa+ kwa nyumba imeneyo kunali kwamkokomo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena