20 Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.+ Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake. Bambo sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za mwana wake.+ Chilungamo cha munthu wolungama chidzakhala pa iye,+ ndipo zoipa za munthu woipa zidzakhala pamutu pa woipayo.+
12 Bzalani mbewu za chilungamo+ ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha.+ Limani munda panthaka yabwino+ pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova, kufikira iye atabwera+ ndi kukupatsani malangizo onena za chilungamo.+