Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 18:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Chotero Yehova anati: “Kudandaula kokhumudwa chifukwa cha Sodomu ndi Gomora+ kwamveka kwambiri, ndipo tchimo lawo n’lalikulu kwambiri.+

  • Genesis 19:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndiyeno Yehova anavumbitsa sulufule ndi moto kuchokera kwa Yehova kumwamba, kuvumbira pa Sodomu ndi Gomora.+

  • Deuteronomo 29:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Adzanena mawuwo akadzaonanso sulufule, mchere+ ndi kutentha,+ moti m’dzikomo simungabzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, mofanana ndi Sodomu ndi Gomora,+ Adima+ ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga mu ukali ndi mkwiyo wake.+

  • Deuteronomo 32:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,

      Ndi kuminda ya m’mapiri a ku Gomora.+

      Zipatso zawo za mphesa ndi zakupha,

      Ndipo ndi zowawa.+

  • Yesaya 1:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Imvani mawu a Yehova,+ inu olamulira ankhanza+ a ku Sodomu.+ Mvetserani malamulo a Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora.

  • Yesaya 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,+ ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo lofanana ndi la Sodomu.+ Iwo sanalibise. Tsoka kwa iwo, chifukwa adzibweretsera mavuto.+

  • Yeremiya 23:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa.+ Iwo achita chigololo+ ndi kuchita zinthu mwachinyengo.+ Alimbikitsa anthu ochita zoipa kuti aliyense asafooke ndi kusiya+ kuchita zoipa zake. Kwa ine, onsewo akhala ngati Sodomu+ ndipo anthu okhala mumzindawu akhala ngati Gomora.”+

  • Yuda 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yozungulira mizinda imeneyi,+ inalandira chilango cha moto wosatha,+ motero yaikidwa monga chitsanzo chotichenjeza.+ Anthu ake anachita mofanana ndi amene tatchula aja, pochita dama loipitsitsa ndiponso pogonana m’njira imene si yachibadwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena