Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:49
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 49 “Yehova adzautsa mtundu wakutali, kumalekezero a dziko,+ mtundu umene chilankhulo chake sudzachimva.+ Mtunduwo udzakuukira monga mmene chiwombankhanga chimakhwathulira nyama yake,+

  • 2 Mafumu 15:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 M’masiku a Peka mfumu ya Isiraeli, Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri+ inabwera n’kulanda Iyoni,+ Abele-beti-maaka,+ Yanoa, Kedesi,+ Hazori,+ Giliyadi,+ ndi Galileya,+ dziko lonse la Nafitali.+ Inatenga anthu a m’madera amenewa n’kupita nawo ku Asuri.+

  • 2 Mafumu 17:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+

  • Yesaya 7:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “M’tsiku limenelo, pogwiritsira ntchito lezala lobwereka la kuchigawo cha ku Mtsinje,*+ pogwiritsira ntchito mfumu ya Asuri,+ Yehova adzameta tsitsi la kumutu ndi tsitsi la m’mapazi, ndipo lezalalo lidzachotseratu ngakhale ndevu.+

  • Yesaya 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 popeza mwanayo asanadziwe kuitana+ kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ anthu adzanyamula chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya n’kupita naye pamaso pa mfumu ya Asuri.”+

  • Yesaya 10:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Eya! Msuri+ ndiye ndodo ya mkwiyo wanga+ komanso chikwapu chosonyezera ukali wanga chimene chili m’dzanja lake.

  • Hoseya 10:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Wina adzapititsa fanolo kudziko la Asuri ndi kukalipereka monga mphatso kwa mfumu yaikulu.+ Efuraimu adzachita manyazi+ ndipo Isiraeli adzachita manyazi ndi zoipa zimene anali kufuna kuchita.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena