2 Mbiri 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 ndipo anthu anga+ otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa+ n’kupemphera,+ n’kufunafuna nkhope yanga,+ n’kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba+ n’kuwakhululukira tchimo lawo+ ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+ Salimo 32:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.] Miyambo 28:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+ Luka 18:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+ 1 Yohane 1:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Mulungu ndi wokhulupirika ndiponso wolungama, chotero tikavomereza machimo athu,+ adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.+
14 ndipo anthu anga+ otchedwa ndi dzina langa+ akadzichepetsa+ n’kupemphera,+ n’kufunafuna nkhope yanga,+ n’kusiya njira zawo zoipa,+ ine ndidzamva ndili kumwamba+ n’kuwakhululukira tchimo lawo+ ndipo ndidzachiritsa dziko lawo.+
5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.]
13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+ koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.+
13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa+ ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’+
9 Mulungu ndi wokhulupirika ndiponso wolungama, chotero tikavomereza machimo athu,+ adzatikhululukira ndi kutiyeretsa ku ntchito zonse zoipa.+