Yobu
7 “Kodi si paja munthu amagwira ntchito yokakamiza+ padziko lapansi?
Ndipo kodi masiku ake sali ngati masiku a munthu waganyu?+
2 Monga kapolo, iye amakhala wefuwefu kufunafuna mthunzi,+
Ndipo ngati munthu waganyu, amadikirira malipiro ake.+
3 Chotero ndalandira miyezi yachabechabe ngati cholowa,+
Ndipo kuvutika usiku uliwonse+ ndiwo malipiro anga.
4 Ndikagona ndimanena kuti, ‘Kodi ndidzuka nthawi yanji?’+
Kukada ndimangokhalira kutembenukatembenuka mpaka m’mawa kuli mbuu.
5 Mnofu wanga wakutidwa ndi mphutsi+ ndipo wamatirira fumbi,+
Khungu langa lang’ambika n’kumatuluka mafinya.+
6 Masiku anga akufulumira+ kuposa mmene chimathamangira chowombera nsalu,
Iwo afika pamapeto popanda chiyembekezo.+
8 Diso la iye amene amandiona silidzandionanso,
Maso anu adzandiyang’ana, koma ine kudzakhala kulibe.+
9 Mtambo umafika kumapeto ake n’kutha.
Chimodzimodzi ndi munthu amene wapita ku Manda,* sadzabwerako.+
11 Choncho, ine sinditseka pakamwa panga.
Ndilankhula chifukwa cha kuvutika mumtima,+
Ndilankhula za nkhawa zanga, chifukwa moyo wanga ukupweteka.
13 Ndikanena kuti, ‘Bedi langa linditonthoza,
Bedi langa lindithandiza kusenza nkhawa zanga,’
14 Inuyo mumandiopseza ndi maloto,
Ndipo mumandichititsa mantha ndi masomphenya.
15 Chotero moyo wanga wasankha kubanika,
Wasankha imfa+ m’malo mwa mafupa angawa.
16 Moyo ndaukana,+ sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.*
Ndisiyeni chifukwa masiku anga ndi ochepa kwambiri.+
17 Kodi munthu ndani+ kuti mumulere,
Ndi kuti muzimuganizira?
18 Iye ndani kuti muzimuganizira m’mawa uliwonse,
Ndi kuti muzimuyesa nthawi zonse?+