18Tsopano Yehova analankhula ndi Aroni kuti: “Iwe ndi ana ako, ndi nyumba yonse ya bambo ako, mudzasenza zolakwa zanu pa malamulo okhudza malo opatulika.+ Iweyo ndi ana ako mudzasenza zolakwa zanu pa malamulo okhudza unsembe wanu.+
24 Iye ananyamula machimo athu+ m’thupi lake pamtengo,+ kuti tilekane ndi machimo+ n’kukhala amoyo m’chilungamo. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+