Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Pa tsiku lotsatira, Mose anati kwa anthuwo: “Inuyo mwachita tchimo lalikulu.+ Choncho ndikwera kupita kwa Yehova kuti mwina ndikakam’chonderera angakukhululukireni tchimo lanu.”+

  • Levitiko 12:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi ikhale nsembe yopsereza, inayo ikhale nsembe yamachimo. Pamenepo wansembe azim’phimbira machimo+ ndipo mkaziyo azikhala woyera.’”

  • Levitiko 16:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Musamapezeke munthu wina mu chihema chokumanako kuyambira pamene iye walowa m’malo oyera kukaphimba machimo kufikira atatulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake,+ a nyumba yake ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+

  • Numeri 15:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Pamenepo wansembe azipereka nsembe yophimba machimo+ a khamu lonse la ana a Isiraeli. Akatero, anthuwo azikhululukidwa cholakwacho chifukwa anachita mosazindikira,+ komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova, ndiponso nsembe yamachimo kwa Yehova pa cholakwa chawocho.

  • Aefeso 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi+ ake, inde, takhululukidwa+ machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.+

  • 1 Timoteyo 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pakuti pali Mulungu mmodzi+ ndi mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu+ ndi anthu.+ Ameneyo ndiye munthuyo Khristu Yesu.+

  • Aheberi 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Chotero, iye anayenera ndithu kukhala ngati “abale” ake m’zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu.+ Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yophimba machimo+ kuti tikhalenso ogwirizana ndi Mulungu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena