15 Kuwonjezera apo, ku Yerusalemu anapanga makina ankhondo opangidwa ndi anthu aluso, oti aziwaika pansanja+ ndi pamakona a mpanda, kuti aziponyera mivi ndi miyala ikuluikulu. Chotero anatchuka+ mpaka kutali kwambiri, popeza anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu.