17Eliya+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi+ analankhula ndi Ahabu kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli+ amene ndimam’tumikira,+ sikugwa mame kapena mvula+ zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.”+
4 Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+