Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 19:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pamenepo phiri la Sinai linafuka utsi ponseponse,+ chifukwa chakuti Yehova anatsikira paphiripo m’moto.+ Utsi wakewo unali kukwera kumwamba ngati utsi wa uvuni,+ ndipo phiri lonse linali kunjenjemera kwambiri.+

  • Ekisodo 20:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:+ “Ana a Isiraeli uwauze kuti, ‘Mwadzionera nokha kuti ine ndalankhula nanu kuchokera kumwamba.+

  • Deuteronomo 4:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pamenepo Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera pakati pa moto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu osaona kalikonse.+

  • Deuteronomo 4:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Chotero musamale moyo wanu,+ chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse+ m’motomo.

  • Deuteronomo 4:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Kodi anthu ena anamvapo mawu a Mulungu akumveka kuchokera pakati pa moto ngati mmene inuyo munawamvera, ndi kukhalabe ndi moyo?+

  • Nehemiya 9:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndiyeno munatsikira paphiri la Sinai+ ndi kulankhula nawo muli kumwamba.+ Munawapatsa zigamulo zowongoka+ ndi malamulo a choonadi,+ mfundo zabwino ndi malangizo abwino.+

  • Aheberi 12:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pakuti simunafike paphiri limene mungathe kulikhudza,+ loyaka moto,+ lokhala ndi mtambo wakuda, mdima wandiweyani komanso lowombedwa ndi mphepo yamkuntho.+

  • Aheberi 12:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Samalani kuti musasiye kumvetsera wolankhulayo.+ Pakuti ngati amene analephera kumvera wopereka chenjezo la Mulungu padziko lapansi sanapulumuke,+ kuli bwanji ifeyo? Nafenso sitidzapulumuka tikachoka kwa iye amene amalankhula ali kumwamba.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena