Deuteronomo 7:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova Mulungu wako adzawapereka ndithu kwa iwe ndipo udzawagonjetse.+ Udzawawononge ndithu+ ndipo usadzachite nawo pangano kapena kuwakomera mtima.+ Oweruza 3:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Mzimu+ wa Yehova unakhala pa iye, ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Siriya m’manja mwake, moti anam’gonjetsa.+ Oweruza 4:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.”+ Ndipo Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira. 2 Mbiri 16:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kodi Aitiyopiya+ ndi Alibiya+ sanali gulu lankhondo lalikulu, la anthu ambiri, magaleta ambiri, ndi okwera pamahatchi ambirinso?+ Chifukwa chakuti munadalira Yehova, kodi iye sanawapereke m’manja mwanu?+ 2 Mbiri 20:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo.+ Khalani m’malo anu, imani chilili+ ndi kuona Yehova akukupulumutsani.+ Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.+ Mawa mupite kukakumana nawo ndipo Yehova akhala nanu.’”+
2 Yehova Mulungu wako adzawapereka ndithu kwa iwe ndipo udzawagonjetse.+ Udzawawononge ndithu+ ndipo usadzachite nawo pangano kapena kuwakomera mtima.+
10 Mzimu+ wa Yehova unakhala pa iye, ndipo anakhala woweruza wa Isiraeli. Atapita kunkhondo, Yehova anapereka Kusani-risataimu mfumu ya Siriya m’manja mwake, moti anam’gonjetsa.+
14 Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.”+ Ndipo Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira.
8 Kodi Aitiyopiya+ ndi Alibiya+ sanali gulu lankhondo lalikulu, la anthu ambiri, magaleta ambiri, ndi okwera pamahatchi ambirinso?+ Chifukwa chakuti munadalira Yehova, kodi iye sanawapereke m’manja mwanu?+
17 Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo.+ Khalani m’malo anu, imani chilili+ ndi kuona Yehova akukupulumutsani.+ Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.+ Mawa mupite kukakumana nawo ndipo Yehova akhala nanu.’”+