Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Uziopa Yehova Mulungu wako+ ndi kum’tumikira,+ ndipo uzilumbira pa dzina lake.+

  • Deuteronomo 10:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Muziopa Yehova Mulungu wanu.+ Muzim’tumikira,+ kum’mamatira+ ndi kulumbira pa dzina lake.+

  • Oweruza 8:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “Anali abale anga, ana a amayi anga. Pali Yehova Mulungu wamoyo, sindikanakuphani mukanawasiya amoyo.”+

  • 1 Samueli 14:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, Mlanditsi wa Isiraeli, munthu amene wachititsa tchimoli ayenera kufa ndithu,+ ngakhale atakhala Yonatani mwana wanga.” Koma panalibe ngakhale munthu mmodzi womuyankha mwa anthu onsewo.

  • 1 Samueli 19:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Sauli anamvera mawu a Yonatani, ndipo analumbira kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ Davide saphedwa.”

  • 1 Samueli 20:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma poyankha Davide analumbira+ kuti: “Bambo ako ayenera kuti akudziwa ndithu kuti iweyo umandikonda.+ Pa chifukwa chimenechi iwo adzanena kuti, ‘Musamuuze zimenezi Yonatani kuti zingamupweteketse mtima.’ Moti ndikunenetsa, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wako,+ imfa ili pafupi kwambiri ndi ine!”+

  • 1 Samueli 25:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Tsopano mbuyanga, ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wanu:+ Yehova wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wamagazi+ komanso kuti musadzipulumutse nokha ndi dzanja lanu.+ Choncho lolani kuti adani anu ndi onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala.+

  • Mateyu 5:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena