18 Nthawi yomweyo, Abigayeli+ anafulumira kutenga mitanda 200 ya mkate, mitsuko iwiri ikuluikulu ya vinyo,+ anapha nkhosa zisanu,+ anatenganso miyezo ya seya isanu ya tirigu wokazinga,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100+ ndi nkhuyu zouma zoumba pamodzi 200+ ndi kuzikweza pa abulu.