Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Usalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+

  • Deuteronomo 16:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama.

  • Salimo 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Sapereka ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

      Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

      Wochita zinthu zimenezi, sadzagwedezeka konse.+

  • Salimo 26:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 M’manja mwa anthu amenewa muli khalidwe lotayirira,+

      Ndipo m’dzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.+

  • Miyambo 29:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pochita zinthu zachilungamo, mfumu imachititsa dziko kulimba,+ koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.+

  • Yesaya 1:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+

  • Yesaya 33:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 “Pali munthu amene amayenda m’chilungamo nthawi zonse,+ amene amalankhula zowongoka,+ amene amakana kupeza phindu mwachinyengo,+ amene salola kuti manja ake alandire chiphuphu,+ amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi, ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zoipa.+

  • Mika 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Atsogoleri a mumzindawo saweruza asanalandire chiphuphu+ ndipo ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro.+ Aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+ Komatu iwo amadalira Yehova ndipo amanena kuti: “Kodi Yehova sali pakati pathu?+ Choncho tsoka silidzatigwera.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena