3 Mitunduyo ndi olamulira asanu ogwirizana+ a Afilisiti,+ Akanani onse,+ ngakhalenso Asidoni+ ndi Ahivi+ okhala m’phiri la Lebanoni,+ kuchokera kuphiri la Baala-herimoni+ mpaka kumalire a dera la Hamati.+
7 “Yehova akufunsa kuti, ‘Inu ana a Isiraeli, kodi simuli ngati ana a Akusi kwa ine? Kodi si ndine amene ndinatulutsa Aisiraeli m’dziko la Iguputo,+ amenenso ndinatulutsa Afilisiti+ ku Kerete komanso Asiriya ku Kiri?’+