Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma ndakusiya ndi moyo+ kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+

  • Deuteronomo 28:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pamenepo mitundu yonse ya anthu padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova,+ ndipo adzachita nanu mantha.+

  • 1 Mafumu 8:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika,+ ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani.+ Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu,+ kuti akuopeni mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.+

  • 1 Mafumu 18:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Pa nthawi+ yopereka nsembe yambewu, Eliya mneneri anayandikira guwa lansembelo n’kunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Isiraeli,+ lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli,+ ndi kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+

  • 2 Mafumu 19:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ chonde tipulumutseni+ m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+

  • Salimo 46:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Gonjerani anthu inu, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu.+

      Ndidzakwezedwa pakati pa anthu a mitundu ina,+

      Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+

  • Yesaya 52:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Yehova waika pamtunda dzanja lake loyera kuti mitundu yonse ione,+ ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.+

  • Danieli 3:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Tsopano ine ndikuika lamulo+ lakuti, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana amene anganene chilichonse chotsutsana ndi Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego ayenera kudulidwa nthulinthuli,+ ndipo nyumba zawo zisandutsidwe zimbudzi za anthu onse,+ pakuti palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa chotere.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena