Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

      Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

      Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

      Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

  • 2 Mafumu 7:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Koma msilikali wothandiza mfumu amene anaigwira ndi dzanja lake,+ anayankha munthu wa Mulungu woonayo, kuti: “Ngakhale Yehova atatsegula zotsekera madzi akumwamba,+ kodi zimenezo zingachitike?”+ Pamenepo Elisa anati: “Uona zimenezi ndi maso ako,+ koma sudya nawo.”+

  • 2 Mbiri 36:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.

  • Yesaya 5:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Chotero monga momwe lawi la moto limanyeketsera mapesi+ komanso monga mmene udzu wouma umanyekera m’malawi a moto, muzu wawo udzawola n’kuyamba kununkha.+ Maluwa awo adzauma n’kuuluzika ngati fumbi, chifukwa akana malamulo a Yehova wa makamu+ ndipo anyoza mawu a Woyera wa Isiraeli.+

  • Yesaya 28:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Tsopano musakhale anthu onyoza+ chifukwa zingwe zanu zingakhale zolimba, pakuti ndamva kuchokera kwa Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ kuti dziko lonse laweruzidwa kuti liwonongedwe.+

  • Nahumu 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena