2 Samueli 8:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Davide anagonjetsanso Amowabu+ ndi kuwayeza ndi chingwe. Iye anawagoneka pansi kuti ayeze zingwe ziwiri ndi kuwapha, ndiponso chingwe chimodzi chathunthu n’kuwasiya amoyo.+ Choncho Amowabu anakhala atumiki a Davide+ ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+ 1 Mbiri 18:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndiyeno Davide anamanga midzi ya asilikali m’dera la Asiriya a ku Damasiko,+ ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho kwa iye.+ Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+ 2 Mbiri 9:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 osawerengera golide wa amalonda oyendayenda,+ amalonda ena amene anali kubweretsa katundu, mafumu onse a Aluya,+ ndi abwanamkubwa a m’dzikolo amene anali kubweretsa golide ndi siliva kwa Solomo. 2 Mbiri 17:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Afilisiti anali kubweretsa+ mphatso ndi ndalama kwa Yehosafati monga msonkho.+ Aluya+ nawonso anali kum’bweretsera ziweto. Ankabweretsa nkhosa zamphongo 7,700 ndi mbuzi zamphongo 7,700.+ 2 Mbiri 26:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndiyeno Aamoni+ anayamba kupereka msonkho+ kwa Uziya. Pomalizira pake, kutchuka kwake+ kunafika mpaka ku Iguputo chifukwa anasonyeza mphamvu zochuluka zedi.
2 Davide anagonjetsanso Amowabu+ ndi kuwayeza ndi chingwe. Iye anawagoneka pansi kuti ayeze zingwe ziwiri ndi kuwapha, ndiponso chingwe chimodzi chathunthu n’kuwasiya amoyo.+ Choncho Amowabu anakhala atumiki a Davide+ ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+
6 Ndiyeno Davide anamanga midzi ya asilikali m’dera la Asiriya a ku Damasiko,+ ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho kwa iye.+ Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+
14 osawerengera golide wa amalonda oyendayenda,+ amalonda ena amene anali kubweretsa katundu, mafumu onse a Aluya,+ ndi abwanamkubwa a m’dzikolo amene anali kubweretsa golide ndi siliva kwa Solomo.
11 Afilisiti anali kubweretsa+ mphatso ndi ndalama kwa Yehosafati monga msonkho.+ Aluya+ nawonso anali kum’bweretsera ziweto. Ankabweretsa nkhosa zamphongo 7,700 ndi mbuzi zamphongo 7,700.+
8 Ndiyeno Aamoni+ anayamba kupereka msonkho+ kwa Uziya. Pomalizira pake, kutchuka kwake+ kunafika mpaka ku Iguputo chifukwa anasonyeza mphamvu zochuluka zedi.