Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 19:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Iye anaika moyo wake pangozi*+ n’kupha Mfilisiti uja,+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu+ kwa Aisiraeli onse. Inuyo munaona zimenezi zikuchitika, ndipo munasangalala. Ndiye n’chifukwa chiyani mukufuna kuchimwira magazi osalakwa, mwa kupha Davide+ popanda chifukwa?”+

  • Salimo 38:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Iwo anali kundibwezera choipa m’malo mwa chabwino,+

      Ndikamayesetsa kuchita chabwino anali kunditsutsa.+

  • Salimo 109:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Ndikawachitira zabwino amandibwezera zoipa,+

      Ndikawasonyeza chikondi amandibwezera chidani.+

  • Yeremiya 18:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Kodi zabwino amazibwezera ndi zoipa?+ Kumbukirani nthawi zonse zija pamene ndinaima pamaso panu kuwalankhulira zabwino kuti muwachotsere mkwiyo wanu.+ Koma iwo tsopano andikumbira mbuna.+

  • Yohane 10:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Yesu anawauza kuti: “Ndakuonetsani ntchito zambiri zabwino zochokera kwa Atate. Tsopano mukundiponya miyala chifukwa cha ntchito iti mwa zimenezi?”

  • Yohane 18:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndalankhula molakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati ndalankhula moyenera, n’chifukwa chiyani ukundimenya?”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena