9 “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+
2 Chotero iye anapita kukaonekera kwa Asa n’kumuuza kuti: “Tamverani mfumu Asa ndi anthu onse a fuko la Yuda ndi Benjamini. Yehova akhala nanu inuyo mukapitiriza kukhala naye.+ Mukamufunafuna+ iye adzalola kuti mum’peze, koma mukamusiya nayenso adzakusiyani.+