21 Chotero ana awo muwakhaulitse ndi njala yaikulu,+ ndipo aphedwe ndi lupanga.+ Akazi awo akhale amasiye ndipo ana a akaziwo afe.+ Amuna awo afe ndi mliri woopsa ndipo anyamata awo aphedwe ndi lupanga pa nkhondo.+
31 “‘Phokoso lidzamveka kumalekezero a dziko lapansi, pakuti Yehova akufuna kuimba mlandu mitundu ya anthu.+ Iye mwini adzalimbana ndi anthu onse powaweruza.+ Anthu oipa adzawapha ndi lupanga,’+ watero Yehova.