Ekisodo 14:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+ Yoswa 2:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ Tinamvanso za mmene munaphera+ mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya kwa Yorodano. Nehemiya 9:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+ Salimo 66:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,+Anthu anawoloka mtsinje mwa kuyenda ndi mapazi awo.+Pamenepo tinayamba kusangalala mwa iye.+ Salimo 78:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,+Ndipo anaimitsa madzi kukhala ngati khoma.+ Salimo 136:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Yamikani amene anagawa pakati Nyanja Yofiira:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+
10 Tinamva za mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamaso panu, mutatuluka m’dziko la Iguputo.+ Tinamvanso za mmene munaphera+ mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya kwa Yorodano.
11 Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+
6 Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,+Anthu anawoloka mtsinje mwa kuyenda ndi mapazi awo.+Pamenepo tinayamba kusangalala mwa iye.+
13 Yamikani amene anagawa pakati Nyanja Yofiira:+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+