-
1 Mafumu 8:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga, pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako asamale mayendedwe awo mwa kuyenda pamaso panga monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’
-
-
2 Mbiri 6:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Tsopano inu Yehova Mulungu wa Isiraeli, sungani lonjezo limene munalonjeza mtumiki wanu Davide bambo anga lakuti, ‘Anthu a m’banja lako sadzasiya kukhala pamaso panga pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Chofunika n’choti ana ako+ asamale mayendedwe awo mwa kuyenda motsatira malamulo anga+ monga momwe iwe wayendera pamaso panga.’+
-
-
Yesaya 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
-