Deuteronomo 16:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama. 1 Samueli 8:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake,+ koma anali okonda kupeza phindu mwachinyengo,+ ndipo anali kulandira ziphuphu+ ndi kupotoza chiweruzo.+ Miyambo 1:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Umu ndi mmene zimakhalira njira za aliyense wopeza phindu mwachinyengo.+ Phindulo limachotsa moyo wa eni akewo.+ Mlaliki 7:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mphatso+ ikhoza kuwononga mtima wa munthu.+ Yesaya 1:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+
19 Usamapotoze chiweruzo.+ Usamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ ndi kupotoza mawu a anthu olungama.
3 Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake,+ koma anali okonda kupeza phindu mwachinyengo,+ ndipo anali kulandira ziphuphu+ ndi kupotoza chiweruzo.+
19 Umu ndi mmene zimakhalira njira za aliyense wopeza phindu mwachinyengo.+ Phindulo limachotsa moyo wa eni akewo.+
7 Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mphatso+ ikhoza kuwononga mtima wa munthu.+
23 Akalonga ako ndi aliuma ndipo ndi anzawo a mbala.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu+ ndipo amafunafuna mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+