Genesis 24:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Kenako, ngamila zija zitatha kumwa, mlendoyo anatenga ndolo yagolide yovala pamphuno+ yolemera hafu ya sekeli, ndi zibangili ziwiri+ zagolide zoti Rabeka azivala m’mikono, zolemera masekeli 10, Ekisodo 32:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pamenepo Aroni anawauza kuti: “Vulani ndolo* zagolide+ zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mubwere nazo kwa ine.” Ezekieli 16:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Ndinakuvekanso zokongoletsera ndi zibangili+ m’manja mwako ndipo ndinakuveka mkanda+ m’khosi mwako. Hoseya 2:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndiyeno ndidzamuimba mlandu+ chifukwa cha masiku amene anapembedza zifaniziro za Baala+ zimene anali kuzifukizira nsembe zautsi.+ Nthawi imeneyi anali kuvala mphete* yake ndi zinthu zake zodzikongoletsera.+ Iye anali kutsatira amuna omukonda kwambiri+ ndipo ine anandiiwala,’+ watero Yehova.
22 Kenako, ngamila zija zitatha kumwa, mlendoyo anatenga ndolo yagolide yovala pamphuno+ yolemera hafu ya sekeli, ndi zibangili ziwiri+ zagolide zoti Rabeka azivala m’mikono, zolemera masekeli 10,
2 Pamenepo Aroni anawauza kuti: “Vulani ndolo* zagolide+ zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mubwere nazo kwa ine.”
11 Ndinakuvekanso zokongoletsera ndi zibangili+ m’manja mwako ndipo ndinakuveka mkanda+ m’khosi mwako.
13 Ndiyeno ndidzamuimba mlandu+ chifukwa cha masiku amene anapembedza zifaniziro za Baala+ zimene anali kuzifukizira nsembe zautsi.+ Nthawi imeneyi anali kuvala mphete* yake ndi zinthu zake zodzikongoletsera.+ Iye anali kutsatira amuna omukonda kwambiri+ ndipo ine anandiiwala,’+ watero Yehova.