Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 “‘Musadzidetse ndi chilichonse cha zinthu zimenezi, chifukwa mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu yadzidetsa ndi zonse zimenezi.+

  • Numeri 35:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+

  • 2 Mbiri 33:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma Manase+ anapitiriza kunyengerera Yuda+ ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.+

  • Yeremiya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.”+

      Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+

      Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+

  • Yeremiya 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa+ ndipo m’nyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ watero Yehova.

  • Maliro 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+

      Amene anakhetsa magazi a anthu olungama a mumzindawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena