8 Ndidzapha anthu a ku Asidodi+ pamodzi ndi wogwira ndodo yachifumu wa ku Asikeloni.+ Ndidzalanga+ Ekironi+ ndipo ndidzafafaniza otsala mwa Afilisiti,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’
5 “Tsoka kwa anthu okhala m’chigawo cha m’mphepete mwa nyanja, mtundu wa Akereti.+ Yehova wakudzudzulani anthu inu. Iwe Kanani, dziko la Afilisiti, nawenso ndidzakuwononga, kotero kuti m’dziko lako simudzatsala munthu aliyense.+