Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 20:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Choncho ndinatenga mdzakazi wanga ndi kum’duladula, n’kutumiza ziwalozo m’dera lililonse la cholowa cha Isiraeli.+ Ndinatero chifukwa iwo anachita khalidwe lotayirira+ komanso chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli.+

  • Salimo 26:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 M’manja mwa anthu amenewa muli khalidwe lotayirira,+

      Ndipo m’dzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.+

  • Miyambo 10:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Kwa wopusa, kusonyeza khalidwe lotayirira kuli ngati masewera,+ koma nzeru zimakhala ndi munthu wozindikira.+

  • Yeremiya 13:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Chigololo chako,+ kumemesa* kwako,+ khalidwe lako lotayirira la uhule, zonsezi zidzaonekera. Ndaona zinthu zako zonyansa pamapiri kuthengo.+ Tsoka kwa iwe Yerusalemu! Sungakhale woyera.+ Kodi udzakhalabe wosayera kufikira liti?”+

  • Ezekieli 16:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Tsopano ine ndidzakutambasulira dzanja langa+ ndipo ndidzakuchepetsera gawo lako.+ Ndidzakupereka ku zilakolako+ za akazi odana nawe,+ ana aakazi a Afilisiti,+ akazi amene akuchita manyazi ndi khalidwe lako lotayirira.+

  • 2 Petulo 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma anapulumutsa Loti, munthu wolungama+ amene anavutika mtima kwambiri ndi kulowerera kwa anthu ophwanya malamulo mu khalidwe lawo lotayirira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena