Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 28:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mtsogoleri amene ali wosazindikira kwenikweni amakhalanso wakatangale kwambiri,+ koma munthu wodana ndi phindu lachinyengo+ adzachulukitsa masiku ake.

  • Yesaya 32:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+ ndipo akalonga+ adzalamuliranso mwachilungamo.

  • Yesaya 60:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide.+ M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo. Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati wokuyang’anira,+ ndi chilungamo kuti chikhale ngati wokupatsa ntchito.+

  • Yeremiya 22:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 ‘Ndithudi, maso ako ndi mtima wako sizikulakalaka china chilichonse koma phindu lachinyengo,+ anthu osalakwa kuti ukhetse magazi awo+ komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda.’

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Ezekieli 22:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Atsogoleri a mumzindawo ali ngati mimbulu yomwe ikukhadzula nyama. Iwo akukhetsa magazi+ ndiponso kuwononga miyoyo n’cholinga chopeza phindu mwachinyengo.+

  • Ezekieli 46:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mtsogoleri wa anthu asamatenge cholowa chilichonse cha anthu ndi kuwakakamiza kuchoka m’malo awo.+ Ana ake aamuna aziwapatsa cholowa kuchokera pamalo amene ali nawo, kuti anthu anga asamwazikane ndi kuchoka m’malo awo.’”+

  • Mika 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ine ndinapitiriza kunena kuti: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo ndi inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi si inu oyenera kudziwa chilungamo?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena