Yesaya 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+ Yesaya 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+ Yeremiya 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Ezekieli 17:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Mitengo yonse yamthengo idzadziwa kuti ine Yehova+ ndatsitsa mtengo waukulu+ ndi kukweza mtengo wonyozeka,+ ndaumitsa mtengo wauwisi+ ndi kuchititsa maluwa mtengo umene unali wouma. Ine Yehova ndanena ndi kuchita zimenezi.”’”+ Ezekieli 37:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 “‘“Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo.+ Onse adzakhala ndi m’busa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga+ ndipo adzasunga malamulo anga+ ndi kuwatsatira.+ Zekariya 12:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Pa tsiku limenelo, Yehova adzatchinjiriza anthu okhala mu Yerusalemu.+ Munthu amene wapunthwa pa tsiku limenelo, adzakhala wamphamvu ngati Davide.+ Nyumba ya Davide idzawatsogolera ngati Mulungu,+ ndiponso ngati mngelo wa Yehova.+ Luka 1:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Tsopano mvetsera! Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna.+ Udzam’patse dzina lakuti Yesu.+
6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+
11 Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+
5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+
24 Mitengo yonse yamthengo idzadziwa kuti ine Yehova+ ndatsitsa mtengo waukulu+ ndi kukweza mtengo wonyozeka,+ ndaumitsa mtengo wauwisi+ ndi kuchititsa maluwa mtengo umene unali wouma. Ine Yehova ndanena ndi kuchita zimenezi.”’”+
24 “‘“Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo.+ Onse adzakhala ndi m’busa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga+ ndipo adzasunga malamulo anga+ ndi kuwatsatira.+
8 Pa tsiku limenelo, Yehova adzatchinjiriza anthu okhala mu Yerusalemu.+ Munthu amene wapunthwa pa tsiku limenelo, adzakhala wamphamvu ngati Davide.+ Nyumba ya Davide idzawatsogolera ngati Mulungu,+ ndiponso ngati mngelo wa Yehova.+
31 Tsopano mvetsera! Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna.+ Udzam’patse dzina lakuti Yesu.+