45 “Matemberero onsewa+ adzakugwera, kukutsatira ndi kukupeza kufikira utafafanizika,+ chifukwa sunamvere mawu a Yehova Mulungu wako mwa kusunga malamulo ndi mfundo zake zimene anakupatsa.+
4Tamverani mawu a Yehova inu ana a Isiraeli. Yehova ali ndi mlandu ndi anthu okhala m’dzikoli,+ chifukwa m’dzikoli mulibe choonadi,+ kukoma mtima kosatha, ndiponso anthu a m’dzikoli amachita zinthu ngati kuti sadziwa Mulungu.+