KALATA YACHIWIRI YOPITA KWA ATESALONIKA
1 Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano* komanso Timoteyo+ ndipo ndikulembera mpingo wa Atesalonika, womwe ndi wogwirizana ndi Mulungu Atate wathu komanso Ambuye Yesu Khristu kuti:
2 Kukoma mtima kwakukulu komanso mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.
3 Tikuyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Zimenezi nʼzoyenera chifukwa chikhulupiriro chanu chikukula kwambiri ndipo chikondi chimene aliyense amasonyeza kwa mnzake chikuwonjezereka.+ 4 Choncho ifeyo timanyadira+ tikamanena za inu ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chimene mumasonyeza mukamazunzidwa komanso kulimbana ndi mavuto* amene mukukumana nawo.*+ 5 Umenewu ndi umboni wakuti Mulungu amaweruza molungama ndipo chifukwa cha zimenezi mwaonedwa kuti ndinu oyenerera Ufumu wa Mulungu, umene mukuuvutikira.+
6 Popeza Mulungu ndi wolungama, iye adzapereka chilango kwa amene amachititsa kuti muzizunzika.+ 7 Koma inu amene mukuvutika mudzapatsidwa mpumulo pamodzi ndi ife pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere*+ kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu+ 8 mʼmoto walawilawi. Pa nthawi imeneyo adzabwezera chilango kwa anthu osadziwa Mulungu komanso kwa anthu amene samvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.+ 9 Anthu amenewa adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya+ ndipo adzachotsedwa pamaso pa Ambuye moti sadzaonanso mphamvu zake zaulemerero. 10 Zimenezi zidzachitika pa nthawi imene adzabwere kudzalandira ulemerero limodzi ndi oyera ake. Pa tsiku limenelo, onse amene anamukhulupirira adzamuyangʼanitsitsa mwachidwi, chifukwa munakhulupirira umboni umene tinapereka kwa inu.
11 Pa chifukwa chimenechi, timakupemphererani nthawi zonse kuti Mulungu wathu akuoneni kuti ndinu oyenereradi kuitanidwa ndi iye.+ Mulungu achite mokwanira zinthu zonse zabwino zimene akufuna kuchita ndi mphamvu zake, ndipo achititse kuti ntchito zanu zachikhulupiriro zikhale zopindulitsa. 12 Timakupemphererani kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezeke mwa inu komanso kuti inu mulemekezeke mwa iye, mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.
2 Komabe abale, pa nkhani yokhudza kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu+ komanso kusonkhanitsidwa kwathu kwa iye,+ tikukupemphani kuti 2 musalole kuti wina aliyense asinthe maganizo anu omwe ndi olondola. Musasokonezeke ngati wina atanena kuti tsiku la Yehova*+ lafika, ngakhale atanena kuti uthengawo ndi wochokera kwa Mulungu,+ kapena atanena kuti anawerenga mʼkalata imene anthu ena akunena kuti ife ndi amene tinalemba.
3 Musalole kuti aliyense akusocheretseni* mwa njira iliyonse chifukwa tsikulo lisanafike, choyamba mpatuko+ ukuyenera kuchitika ndiponso munthu wosamvera malamulo,+ amene ndi mwana wa chiwonongeko,+ akuyenera kuonekera. 4 Iye amatsutsa komanso kudzikweza pamwamba pa aliyense wotchulidwa kuti mulungu kapena chilichonse chimene chimalambiridwa,* moti amakhala pansi mʼkachisi wa Mulungu nʼkumadzionetsa poyera kuti iye ndi mulungu. 5 Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu ndinkakuuzani zimenezi?
6 Ndipo inu mukudziwa chimene chikuchititsa kuti panopa asaonekere, kuti adzaonekere pa nthawi yake yoyenera. 7 Zoona, kuipa kwa munthu ameneyu, komwe ndi kwachinsinsi, kwayamba kale kugwira ntchito.+ Koma kuipa kumeneku kupitiriza kukhala chinsinsi mpaka amene akumulepheretsa atachoka. 8 Kenako, wosamvera malamuloyo adzaonekera poyera. Ambuye Yesu adzathetsa wosamvera malamuloyu ndi mzimu wamʼkamwa mwake+ ndipo adzamuwonongeratu pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekere.+ 9 Koma kukhalapo kwa wosamvera malamuloyo kukutheka ndi mphamvu za Satana.+ Iye akuchita ntchito iliyonse yamphamvu, zizindikiro zabodza, zodabwitsa+ 10 komanso akugwiritsa ntchito njira iliyonse yachinyengo+ kuti apusitse amene akupita kukawonongedwa. Izi zidzakhala chilango kwa iwo chifukwa sanalandire komanso kukonda choonadi kuti adzapulumuke. 11 Nʼchifukwa chake Mulungu walola kuti iwo apusitsidwe ndi ziphunzitso zabodza nʼcholinga choti azikhulupirira bodza,+ 12 kuti onsewo adzaweruzidwe chifukwa sanakhulupirire choonadi koma ankasangalala ndi zosalungama.
13 Komabe, tiyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale amene Yehova* amakukondani, chifukwa Mulungu anakusankhani kuchokera pachiyambi+ kuti mudzapulumuke. Anachita zimenezi pokuyeretsani+ ndi mzimu wake komanso chifukwa munakhulupirira choonadi. 14 Anakuitanani ku chipulumutso chimenechi kudzera mu uthenga wabwino umene tikulengeza, kuti mudzapeze ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 15 Choncho abale, khalani olimba+ ndipo gwirani mwamphamvu miyambo imene munaphunzitsidwa,+ kaya kudzera mu uthenga wapakamwa kapena mʼkalata yochokera kwa ife. 16 Komanso Ambuye wathu Yesu Khristu ndiponso Mulungu Atate wathu, amene anatikonda+ ndipo salephera kutilimbikitsa komanso anatipatsa chiyembekezo chabwino,+ kudzera mwa kukoma mtima kwakukulu, 17 alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani kuti nthawi zonse muzichita komanso kulankhula zinthu zabwino.
3 Pomaliza abale, pitirizani kutipempherera+ kuti mawu a Yehova* apitirize kufalikira mofulumira+ komanso kulemekezedwa ngati mmene akuchitira pakati panu. 2 Muzitipemphereranso kuti tipulumutsidwe kwa anthu oipa kwambiri,+ chifukwa si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro.+ 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipayo. 4 Komanso monga otsatira a Ambuye, tili ndi chikhulupiriro mwa inu kuti mukutsatira malangizo amene tinakupatsani ndipo mupitiriza kuwatsatira. 5 Ambuye apitirize kutsogolera mitima yanu kuti muzikonda Mulungu+ komanso kuti muzipirira+ chifukwa cha Khristu.
6 Tsopano abale tikukupatsani malangizo mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti muzipewa mʼbale aliyense amene akuyenda mosalongosoka+ komanso amene akuchita zinthu zosagwirizana ndi malangizo amene* tinakupatsani.*+ 7 Ndipotu inuyo mukudziwa zimene mukuyenera kuchita potitsanzira,+ chifukwa sitinachite zinthu zosalongosoka pakati panu, 8 kapena kudya chakudya cha wina aliyense kwaulere.*+ Mʼmalomwake, tinagwira ntchito mwakhama komanso ndi mphamvu zathu zonse usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza.+ 9 Sikuti tinachita zimenezi chifukwa choti tilibe ulamuliro wokupemphani kuti mutithandize,+ koma tinkafuna kuti tikupatseni chitsanzo choti muzitsanzira.+ 10 Ndipotu pamene tinali ndi inu, tinkakupatsani lamulo lakuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 11 Chifukwa tikumva kuti ena akuyenda mosalongosoka pakati panu,+ sakugwira ntchito nʼkomwe, koma akulowerera nkhani zimene sizikuwakhudza.+ 12 Anthu otero tikuwalamula ndi kuwachonderera mwa Ambuye Yesu Khristu kuti azigwira ntchito mwakhama popanda kulowerera nkhani za anthu ena ndipo azidya chakudya chimene iwowo achigwirira ntchito.+
13 Koma inuyo abale, musasiye kuchita zabwino. 14 Koma ngati wina sakumvera mawu athu amene ali mʼkalatayi, muikeni chizindikiro ndipo musiye kuchitira naye zinthu limodzi+ kuti achite manyazi. 15 Komabe musamuone ngati mdani, koma pitirizani kumulangiza+ monga mʼbale.
16 Tsopano Ambuye wamtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mʼnjira iliyonse.+ Ambuye akhale nanu nonsenu.
17 Landirani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa.+ Nthawi zonse ndimalemba chonchi mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembera.
18 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu nonsenu.
Amene amadziwikanso kuti Sila.
Kapena kuti, “masautso.”
Kapena kuti, “mukuwapirira.”
Kapena kuti, “adzaululike.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “akunyengerereni.”
Kapena kuti, “chimene chimalemekezedwa.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “mwambo umene.”
Mabaibulo ena amati, “tinawapatsa.”
Kapena kuti, “osalipira.”