1 Akorinto
16 Tsopano ponena za chopereka+ chopita kwa oyerawo,+ inunso tsatirani malangizo amene ndinapereka ku mipingo ya ku Galatiya.+ 2 Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake, kuti ndikadzafika, zopereka zisadzaperekedwe pa nthawi imeneyo. 3 Koma ndikadzafika kumeneko, amuna alionse amene mungawavomereze m’makalata,+ ndidzawatuma kuti adzapititse mphatso yanu yachifundoyo ku Yerusalemu. 4 Komabe, ngati kudzakhala kofunika kuti inenso ndidzapite, tidzapitira limodzi.
5 Ndidzafika kwa inu pochokera ku Makedoniya, pakuti ndipita ku Makedoniya.+ 6 Mwina ndidzakhala nanu pang’ono kumeneko, ngakhalenso kwa nyengo yonse yachisanu, kuti mudzandiperekeze+ kumene ndizidzapitako. 7 Pakuti sindikufuna kukuonani panopo mongodutsa chabe, koma ndikufuna kuti ndidzakhale nanu kanthawi ndithu,+ ngati Yehova+ alola.+ 8 Koma ndikhalabe kuno ku Efeso+ mpaka chikondwerero cha Pentekosite, 9 pakuti khomo lalikulu la mwayi wautumiki landitsegukira,+ koma pali otsutsa ambiri.
10 Komabe, Timoteyo+ akadzafika mudzaonetsetse kuti asadzakhale ndi mantha pakati panu, pakuti iye akuchita ntchito ya Yehova,+ mmenenso ine ndikuchitira. 11 Choncho pasadzapezeke munthu womuderera.+ Mudzamuperekeze mu mtendere kuti adzafike kwa ine kunoko, pakuti ineyo ndikumuyembekezera pamodzi ndi abale.
12 Tsopano kunena za m’bale wathu Apolo,+ ndinamuchonderera kwambiri kuti abwere kwanuko pamodzi ndi abale, koma iye sanafune kubwera pa nthawi ino. Adzabwera akadzapeza mpata.
13 Khalani maso,+ limbani m’chikhulupiriro,+ pitirizani kuchita chamuna,+ khalani amphamvu.+ 14 Zonse zimene mukuchita, muzichite mwachikondi.+
15 Tsopano ndikukulimbikitsani mokudandaulirani, abale, kuti: Mukudziwa kuti banja la Sitefana ndilo chipatso choyambirira+ mu Akaya ndi kuti anadzipereka kutumikira oyera.+ 16 Inunso pitirizani kudzipereka kwa anthu ngati amenewo, ndi kwa aliyense wogwirizana nafe pa ntchitoyi, ndiponso wogwira ntchito molimbika.+ 17 Koma ndikusangalala kuti Sitefana+ ndi Fotunato ndi Akayiko ali kuno ndi ine, pakuti alowa m’malo mwanu. 18 Pakuti atsitsimutsa mtima wanga+ ndi wanunso. Chotero, anthu otere muziwalemekeza.+
19 Mipingo ya ku Asia ikupereka moni.+ Akula ndi Purisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m’nyumba mwawo,+ akupereka moni wochokera pansi pa mtima kwa inu nonse, mwa Ambuye. 20 Abale onse akukupatsani moni. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.+
21 Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa, ineyo Paulo.+
22 Ngati wina aliyense sakonda Ambuye, atembereredwe.+ Inde, idzani Ambuye!+ 23 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu kukhale nanu. 24 Nonsenu landirani chikondi changa mwa Khristu Yesu.