14 “Ine ndidzawawombola ku Manda*+ ndiponso ku imfa.+ Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+ Iwe Manda amene umawononga, kodi uli kuti?+ Koma Efuraimu sindimumverabe chisoni.+
31 Choncho pokhala mneneri, iye anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka kwa Khristu. Ananeneratu kuti iye sanasiyidwe m’Manda, komanso kuti thupi lake silinavunde.+