-
Ezekieli 42:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Zipinda zodyeramo za kumpoto ndi za kum’mwera zimene zili moyang’anizana ndi mpata waukulu+ ndi zopatulika. M’zipinda zimenezi, ansembe otumikira+ Yehova amadyeramo zinthu zopatulika koposa.+ Mmenemo amaikamo zinthu zopatulika koposa, nsembe yambewu, nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula, chifukwa malo amenewa ndi oyera.+
-