-
Oweruza 9:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Mulungu analola zimenezi kuti chiwawa chimene anachitira ana aamuna 70 a Yerubaala chiwabwerere pamutu pawo,+ ndi kuti aike magazi a anawo pa Abimeleki m’bale wawo chifukwa ndiye anawapha.+ Analolanso zimenezi kuti chiwawacho chibwerere pamutu pa nzika za Sekemu, chifukwa zinalimbikitsa+ Abimeleki kuti aphe abale ake.
-
-
1 Samueli 25:39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Ndiyeno Davide anamva kuti Nabala wamwalira. Atatero, iye anati: “Adalitsike Yehova amene wandiweruzira mlandu+ ndi kundimasula ku chitonzo+ cha Nabala, komanso wagwira ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa.+ Yehova wabwezera zoipa za Nabala pamutu pake!”+ Pamenepo Davide anatumiza anthu kuti akamufunsirire Abigayeli, kuti akhale mkazi wake.+
-