22 Ndiye zinali kuchitika kuti, pa tsiku lankhondo panalibe munthu aliyense mwa anthu amene anali ndi Sauli ndi Yonatani, amene anali ndi lupanga+ kapena mkondo m’manja mwake. Koma Sauli+ yekha ndi mwana wake Yonatani ndi amene anali ndi zida.
49 Ana aamuna a Sauli anali Yonatani,+ Isivi ndi Malikisuwa.+ Ndipo mayina a ana ake awiri aakazi ndi awa: Woyamba kubadwa anali Merabu,+ ndipo wamng’ono anali Mikala.+
7 Koma mfumu inamvera chisoni Mefiboseti+ mwana wamwamuna wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha lumbiro+ limene Davideyo ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pakati pawo pamaso pa Yehova.