Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+

  • 1 Mafumu 8:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Yehova anakwaniritsa mawu amene ananena,+ kuti ineyo ndilowe m’malo mwa Davide bambo anga n’kukhala pampando wachifumu wa Isiraeli,+ monga momwe Yehova ananenera, ndiponso kuti ndimange nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.+

  • Salimo 132:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova walumbira kwa Davide,+

      Ndithudi sadzabweza mawu ake akuti:+

      “Ndidzaika pampando wako wachifumu+

      Chipatso cha mimba yako.+

  • Yesaya 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+

  • Yesaya 11:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+

  • Mateyu 21:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma khamu la anthu, limene linali patsogolo pake ndi m’mbuyo mwake linali kufuula kuti: “M’pulumutseni+ Mwana wa Davide!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!*+ M’pulumutseni kumwambamwambako!”+

  • Mateyu 22:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+

  • Luka 1:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.+ Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu+ wa Davide atate wake.+

  • Yohane 7:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 Kodi Malemba sanena kuti Khristu adzatuluka mwa ana a Davide,+ komanso mu Betelehemu+ mudzi umene Davide anali kukhala?”+

  • Machitidwe 2:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Iye anali mneneri, ndipo anali kudziwa kuti Mulungu anam’lonjeza mwa lumbiro, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi mwa zipatso za m’chiuno mwake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena