Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Pa chiyambi,+ Mulungu+ analenga+ kumwamba ndi dziko lapansi.+

  • Deuteronomo 10:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye.+ Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa,+ amene sakondera+ munthu aliyense ndipo salandira chiphuphu.+

  • Deuteronomo 32:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,+

      Ndipo adani athu angavomereze zimenezi.+

  • Ezara 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+

  • Salimo 145:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+

      Ndipo ukulu wake ndi wosasanthulika.+

  • Danieli 2:47
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Mfumuyo inauza Danieli kuti: “Ndithudi Mulungu wa anthu inu ndi Mulungu wa milungu yonse,+ Ambuye wa mafumu onse+ ndiponso Woulula zinsinsi, chifukwa iwe wakwanitsa kuulula chinsinsi chimenechi.”+

  • Danieli 4:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 “Pamapeto pa masiku amenewa,+ ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba+ ndipo nzeru zanga zinayamba kubwerera. Ndinatamanda Wam’mwambamwamba+ ndipo amene adzakhalapo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza,+ chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

  • Danieli 6:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ine ndikulamula+ kuti m’zigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera ndi kuchita mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Pakuti iye ndi Mulungu wamoyo, amene adzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo ufumu wake+ sudzawonongeka+ komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena