Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 6:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndinali kuonekera kwa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo+ monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse+ kwa iwo.

  • Ekisodo 33:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Ndipo anawonjezera kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angandione n’kukhalabe ndi moyo.”+

  • Deuteronomo 6:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.*+

  • Maliko 10:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yesu anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino?+ Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+

  • Yohane 4:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Mulungu ndiye Mzimu,+ ndipo onse omulambira ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”+

  • Aroma 1:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo,+ makhalidwe a Mulungu osaoneka+ ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu+ wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga+ moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.+

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

  • 1 Timoteyo 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chiphunzitso chimenechi n’chogwirizana ndi uthenga wabwino waulemerero umene anauika m’manja mwanga,+ wochokera kwa Mulungu wachimwemwe.+

  • 1 Timoteyo 2:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pakuti pali Mulungu mmodzi+ ndi mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu+ ndi anthu.+ Ameneyo ndiye munthuyo Khristu Yesu.+

  • Aheberi 9:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.+

  • 1 Yohane 4:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ife tikudziwa ndipo tikukhulupirira za chikondi+ chimene Mulungu ali nacho kwa ife.

      Mulungu ndiye chikondi,+ ndipo munthu amene amapitiriza kusonyeza chikondi,+ amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwirizana+ naye.

  • Chivumbulutso 4:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Zamoyo zinayizo,+ chilichonse chinali ndi mapiko 6.+ Zinali ndi maso thupi lonse ngakhalenso kunsi kwa mapiko.+ Zamoyo zimenezi sizinali kupuma usana ndi usiku. Zinali kunena kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova+ Mulungu, Wamphamvuyonse,+ amene analipo, amene alipo,+ ndi amene akubwera.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena