Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Choncho madziwo anabwereradi,+ ndipo anamiza magaleta ankhondo ndi asilikali apamahatchi a magulu onse ankhondo a Farao, amene analondola Aisiraeli m’nyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+

  • Ekisodo 15:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndipo pamene amuna anali kuimba, Miriamu anathirira mang’ombe kuti:+

      “Imbirani Yehova+ pakuti wakwezeka koposa.+

      Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.”+

  • Yesaya 43:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi, komanso gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu pa nthawi imodzi.+ Iye wanena kuti: “Iwo adzagona pansi,+ sadzadzuka+ ndipo adzatha.+ Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.”+

  • Nahumu 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Yehova wa makamu akuti, “Taona! Ine ndikukuukira,+ ndipo nditentha magaleta ako ankhondo moti padzakhala utsi wambiri.+ Lupanga lidzadya mikango yako yamphamvu.+ Sudzasakanso nyama padziko lapansi,* ndipo mawu a amithenga ako sadzamvekanso.”+

  • Zekariya 12:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pa tsiku limenelo,+ ndidzachititsa hatchi+ iliyonse kudabwa kwambiri, ndipo wokwera pahatchiyo ndidzamuchititsa misala.+ Ndidzatsegula maso anga ndi kuyang’ana nyumba ya Yuda,+ ndipo hatchi iliyonse ya anthu a mitundu ina ndidzaichititsa khungu,” watero Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena