Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Tsopano opani Yehova+ ndi kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika.*+ Chotsani milungu imene makolo anu ankatumikira kutsidya lina la Mtsinje ndi ku Iguputo,+ ndipo tumikirani Yehova.

  • 1 Samueli 12:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Koma muziopa+ Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse m’choonadi.+ Kumbukirani zinthu zazikulu zimene Yehova wakuchitirani.+

  • Salimo 43:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+

      Zimenezi zinditsogolere.+

      Zindifikitse kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+

  • Yesaya 38:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Iye anapemphera kuti: “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+

  • Malaki 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Lamulo la choonadi linali m’kamwa mwake+ ndipo pamilomo pake panalibe zosalungama. Anali kuyenda ndi ine mwamtendere komanso mowongoka mtima,+ ndipo anabweza anthu ambiri panjira zawo zolakwika.+

  • Yohane 8:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Mudzadziwa choonadi,+ ndipo choonadi chidzakumasulani.”+

  • 2 Yohane 4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndikusangalala kwambiri kuti ndapeza ena mwa ana+ anu akuyenda m’choonadi,+ mogwirizana ndi lamulo limene tinalandira kwa Atate.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena