-
Ezekieli 1:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Panali chinachake chooneka ngati utawaleza+ umene umaoneka mumtambo pa tsiku la mvula yamphamvu. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunali kuonekera. Zinali kuoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.
-
-
Danieli 7:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 “Ndiyeno ndinapitiriza kuyang’ana kufikira pamene mipando yachifumu inaikidwa+ ndipo Wamasiku Ambiri+ anakhala pa mpando wake wachifumu. Zovala zake zinali zoyera kwambiri.+ Tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa woyera.+ Mpando wake wachifumu unali kuyaka moto walawilawi,+ ndipo mawilo a mpandowo anali kuyaka moto.+
-