Mikitamu ya Davide.
16 Ndisungeni, inu Mulungu, pakuti ndathawira kwa inu.+
2 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Ubwino wanga sungakupindulitseni,+
3 Koma ungapindulitse oyera amene ali padziko lapansi.
Anthu aulemerero amenewo, ndi amene ndimakondwera nawo.”+
4 Zopweteka zimachuluka kwa anthu amene amati akaona mulungu wina, amamuthamangira.+
Ine sindidzatsanula nsembe zawo zachakumwa zothira magazi,+
Ndipo sindidzatchula dzina lawo ndi milomo yanga.+
5 Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa,+ komanso chikho changa.+
Inu mukundisungira bwino kwambiri cholowa changa.
6 Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.+
Ndithudi, gawo limene ndapatsidwa ndalivomereza.
7 Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+
Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.+
8 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+
Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.+
9 Choncho moyo wanga ukukondwera, ndipo ndidzakhala wosangalala.+
Komanso ndidzakhala wotetezeka.+
10 Pakuti simudzasiya moyo wanga m’Manda.+
Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.+
11 Mudzandidziwitsa njira ya moyo.+
Chifukwa cha nkhope yanu, munthu adzakondwera mokwanira.+
Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.+