Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 98:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Fuulirani Yehova mosangalala chifukwa wapambana, inu nonse anthu a padziko lapansi.+

      Kondwerani, fuulani mosangalala ndi kuimba nyimbo zomutamanda.+

  • Salimo 126:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Pa nthawiyo tinaseka kwambiri,+

      Ndipo lilime lathu linatulutsa mawu okondwa.+

      Pamenepo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:+

      “Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+

  • Miyambo 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mudzi umakondwera chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,+ koma anthu oipa akawonongeka pamakhala mfuu yachisangalalo.+

  • Yesaya 49:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+ Mapiri asangalale ndipo afuule ndi chisangalalo.+ Pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo amamvera chisoni anthu ake osautsidwa.+

  • Yeremiya 51:48
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 48 “Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zidzafuula mosangalala chifukwa cha kugwa kwa Babulo,+ pakuti ofunkha zinthu zake adzafika kuchokera kumpoto,”+ watero Yehova.

  • Chivumbulutso 18:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Kondwerani kumwambako+ chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera,+ inu atumwi,+ ndi inu aneneri, kondwerani chifukwa Mulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena