Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 31:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Atangomaliza kuchita zonsezi, Aisiraeli+ onse amene anali pamenepo anapita kumizinda ya Yuda+ n’kukaphwanya zipilala zopatulika,+ kukadula mizati yopatulika+ ndi kukagwetsa malo okwezeka+ ndi maguwa ansembe+ mu Yuda yense,+ mu Benjamini, mu Efuraimu+ ndi m’Manase+ mpaka kumaliza ntchitoyo. Atatero, ana onse a Isiraeli anabwerera kumizinda yawo, aliyense kumalo ake.

  • 2 Mbiri 34:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Yosiya anagwetsamo maguwa ansembe+ ndi mizati yopatulika.+ Zifaniziro zogoba+ anaziphwanya n’kuziperapera,+ ndipo anagumula zofukizira zonse+ m’dziko lonse la Isiraeli. Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

  • Yeremiya 17:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ngakhale ana awo aamuna akumbukira maguwa awo ansembe ndi mizati yawo yopatulika imene ili pansi pa mtengo waukulu wamasamba ambiri obiriwira, pamwamba pa zitunda zazitali+

  • Ezekieli 36:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ine ndidzakuwazani madzi oyera ndipo mudzakhala oyera. Ndidzakuyeretsani+ pokuchotserani zonyansa zanu zonse+ ndi mafano anu onse onyansa.+

  • Hoseya 8:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Efuraimu wachulukitsa maguwa ansembe ndipo wachimwa.+ Iye wakhala ndi maguwa ansembe ndipo wawonjezera machimo ake.+

  • Hoseya 14:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Efuraimu adzanena kuti, ‘Kodi mafano ndi a chiyaninso kwa ine?’+

      “Ine ndidzamva ndipo ndidzapitirizabe kumuyang’anira.+ Ine ndili ngati mtengo waukulu wa mkungudza wamasamba obiriwira+ ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”

  • Zekariya 13:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova wa makamu wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathetsa mayina a mafano m’dziko lonseli+ ndipo mafanowo sadzakumbukiridwanso. M’dzikoli ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena