-
Ezekieli 6:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Adzadziwa zimenezi mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa+ kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali,+ pansonga zonse za mapiri,+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wanthambi zambiri.+ Amenewa ndiwo malo amene anali kuperekerapo nsembe zafungo lokhazika mtima pansi kwa mafano awo onse onyansa.+
-
-
Ezekieli 20:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Komabe ine ndinawalowetsa m’dziko+ limene ndinawalumbirira nditakweza dzanja langa kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona phiri lililonse lalitali+ ndi mtengo uliwonse wanthambi zambiri, anayamba kupereka nsembe zawo pamenepo+ ndi zopereka zawo zochititsa mseru. Analinso kufukiza nsembe zafungo lokhazika mtima pansi+ ndi kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo.+
-